Hebrews 7:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malamulo a Mose amati ana a Levi, amene ali ansembe, azilandira chachikhumi kwa Aisraele. Ndiye kuti iwo amalandira kwa abale ao, ngakhale abalewo nawonso ndi ana a Abrahamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira ntchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kwa abale ao, angakhale adatuluka m'chuuno cha Abrahamu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono lamulo likuti, ana a Levi amene amakhala ansembe azilandira chakhumi kuchokera kwa Aisraeli, abale awo ngakhale kuti abale awowo ndi ochokera kwa Abrahamu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira nchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa cilamulo, ndiko kwa abaleao, angakhale adaturuka m'cuuno ca Abrahamu;