Hebrews 7:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Melkizedeki sanali m'gulu la zidzukulu za Levi, komabe adalandira chachikhumi kwa Abrahamu. Ndipo adadalitsa Abrahamu, munthu amene anali atalandira malonjezo a Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma iye amene mawerengedwe a chibadwidwe chake sachokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Melikizedeki sanali wochokera kwa Levi, komabe analandira chakhumi kuchokera kwa Abrahamu nadalitsa Abrahamuyo amene analandira malonjezo a Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma iye amene mawerengedwe a cibadwidwe cace sacokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano.