Hebrews 8:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nachi tsono chipangano chimene ndidzachita ndi fuko la Israele atapita masiku ameneŵa,” akutero Ambuye: “Ndidzaika Malamulo anga m'maganizo ao ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Choncho Ine ndidzakhala Mulungu wao, iwowo adzakhala anthu anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israele, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao, ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo; ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu, ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli: Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye, Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo, ndi kulemba mʼmitima mwawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israyeli, Atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao, Ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo; Ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu, Ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu: