Hebrews 8:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sipadzafunikanso kuti wina aliyense aphunzitse mnzake, kapena kuti wina aliyense auze mbale wake kuti, ‘Udziŵe Ambuye’. Pakuti onse adzandidziŵa, kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu mnzake, ndipo yense mbale wake, ndi kuti, Zindikira Ambuye: Pakuti onse adzadziwa Ine, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake, kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye chifukwa onse adzandidziwa, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu mnzace, Ndipo yense mbale wace, ndi kuti, Zindikira Ambuye: Pakuti onse adzadziwa Ine, Kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru wa iwo.