Hebrews 8:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ntchito za chipembedzo zimene iwo amachita, zili ngati chithunzi chongofanizira zenizeni za Kumwamba. Paja zidaateronso ndi Mose: pamene iye adaati amange chihema, Mulungu adaamlangiza kuti, “Upangetu zonse molingana ndi chitsanzo chimene ndidaakuwonetsa paphiri paja.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene atumikira cifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose acenjezedwa m'mene anafuna kupanga cihema: pakuti, Cenjera, ati, ucite zonse monga mwa citsanzoco caonetsedwa kwa iwe m'phiri.