Hebrews 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma monga zilirimu, Yesu adalandira unsembe wopambana kutalitali unsembe wakale uja, monga momwe ndiyenso Nkhoswe ya chipangano chopambana, chifukwa malonjezo ake ngopambana malonjezo a chipangano chakale chija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsopano Iye walandira chitumikiro chomveka koposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsopano iye walandira citumikiro comveka coposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.