Hebrews 8:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sichidzakhala chonga chipangano chimene ndidaachita ndi makolo ao tsiku limene ndidaachita kuŵagwira pa dzanja kuti ndiŵatulutse m'dziko la Ejipito. Chifukwa iwo sadasunge chipangano changa chija, nanenso sindidaŵasamale”, akutero Ambuye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
losati longa pangano ndinalichita ndi makolo ao, tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera atuluke m'dziko la Ejipito; kuti iwo sanakhalabe m'pangano langa, ndipo Ine sindinawasamalira iwo, anena Ambuye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Silidzakhala ngati pangano limene ndinachita ndi makolo awo, pamene ndinawagwira padzanja nʼkuwatulutsa ku Igupto chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija ndipo Ine sindinawasamalire, akutero Ambuye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Losati longa pangano ndinalicita ndi makolo ao, Tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera aturuke m'dziko la Aigupto; Kuti iwo sanakhalabe m'pangano langa, Ndipo loe sindinawasamalira iwo, anena Ambuye,