Hebrews 9:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimangonena za zakudya, za zakumwa, ndi za miyambo yosiyanasiyana ya kasambidwe. Zonsezo ndi malamulo olinga pa zooneka ndi maso chabe, oikidwa kuti azingokhalapo mpaka nthaŵi imene Mulungu adzakonzenso zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inali nkhani ya zakudya, ya zakumwa ndi ya miyambo yosiyanasiyana ya masambidwe. Anali malamulo akunja kokha mpaka pa nthawi imene anakonzanso zonse mwatsopano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyana-siyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.