Hebrews 9:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso changwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza mwa, chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma atafika Kristu, Mkuluwansembe wa zokoma zirinkudza, mwa cihema cacikuru ndi cangwiro coposa, cosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, cosati ca ciiengedweici,