Hebrews 9:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Poyamba Mose adaalengeza kwa Aisraele malamulo onse, motsata Malamulo amene Mulungu adaampatsa. Pambuyo pake adatenga magazi a anaang'ombe amphongo ndi madzi, nawaza pa buku la Malamulo ndi pa anthu onse. Adaachita zimenezi ndi kanthambi ka chitsamba cha hisope, ndiponso ndi ubweya wankhosa wofiira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu once lamulo liri lonse monga mwa cilamulo, anatenga mwazi wa ana a ng'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,