Hebrews 9:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono padaafunika kuti zinthu zongofanizira zenizeni za Kumwamba, ziyeretsedwe ndi miyambo imeneyi. Koma kuti za Kumwamba zenizenizo ziyeretsedwe, padaafunika nsembe zina zoposa zimenezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za m'Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo padafunika kuti 3 zifaniziro za zinthu za m'Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zeni zeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.