Hebrews 9:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkulu wa ansembe onse amaloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chaka ndi chaka atatenga magazi amene sali ake. Koma Khristu sadaloŵe Kumwamba kuti azidzipereka nsembe kaŵirikaŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kosati kuti adzipereke yekha kawirikawiri; monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kosati kuti adzipereke yekha kawiri kawiri; 6 monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika caka ndi caka ndi mwazi wosati wace;