Hebrews 9:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamwamba pa bokosilo panali zithunzi za akerubi oonetsa ulemerero wa Mulungu. Mapiko ao adaaphimbira pa chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nkosatheka tsopano lino kufotokoza zonzezi tsatanetsatane.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitikhoza kunena tsopano paderapadera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi pamwamba pace akerubi a ulemerero akucititsa mthunzi pacotetezerapo; za izi sitikhoza kunena tsopano padera padera.