Hosea 1:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe Aisraele adzachuluka ngati mchenga wakunyanja umene sangathe kuuyesa kapena kuuŵerenga. Pamalo pamene Mulungu adaanena anthuwo kuti “Sindinu anthu anga,” pomweponso adzaŵatchula kuti, “Ana a Mulungu Wamoyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Komabe Aisraeli adzachuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja umene sangathe kuwuyeza kapena kuwuwerenga. Pamalo omwe ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti ‘Ana a Mulungu wamoyo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Angakhale anatero, kuwerenga kwace kwa ana a Israyeli kudzanga mcenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.