Hosea 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Yuda ndi a ku Israele adzaŵasonkhanitsanso pamodzi, ndipo adzadzisankhira mtsogoleri mmodzi. Tsono adzatukuka m'dziko mwao, ndithu tsiku la Yezireele lidzakhala lalikulu kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israele adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkulu mmodzi, nadzakwera kuchoka m'dziko; pakuti tsiku la Yezireele ndi lalikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Israeli adzasonkhananso pamodzi ndipo adzasankha mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka mʼdzikomo, pakuti tsiku la Yezireeli lidzakhala lalikulu kwambiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israyeli adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkuru mmodzi, nadzakwera kucoka m'dziko; pakuti tsiku la Yezreeli ndi lalikuru.