Hosea 1:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Chauta adalankhula koyamba kudzera mwa Hoseya, adamuuza kuti, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubale naye ana omwe adzakhalenso achiwerewere. Pakuti anthu a m'dziko muno akhala osakhulupirika, pakusiya Ine Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova atayamba kuyankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anati kwa Hoseyayo, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubereke naye ana mʼchiwerewere chake pakuti anthu a mʼdziko muno achimwa pochita chigololo choyipitsitsa, posiya Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ciyambi ca kunena kwa Yehova mwa Hoseya, Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wacigololo ndi ana acigololo; pakuti dziko latsata cigololo cokha cokha kuleka kutsata Yehova.