Hosea 1:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti Yezireele. Pakuti patapita kanthaŵi pang'ono, ndidzalanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene iye adaŵapha ku Yezireele, ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Yezireele; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera chilango mwazi wa Yezireele pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti Yezireeli, pakuti ndili pafupi kulanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene anawapha ku Yezireeli ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa iye, Umuche dzina lace Yezreeli; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera cilango mwazi wa Yezreeli pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israyeli.