Hosea 1:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gomeri adatenganso pathupi, nabala mwana wamkazi. Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa,’ pakuti Israele sindidzamkondanso, ndipo sindidzamkhululukiranso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Wosachitidwa-chifundo; pakuti sindidzachitiranso chifundo nyumba ya Israele, kuti ndiwakhululukire konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gomeri anakhala woyembekezeranso ndipo anabereka mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa’ pakuti sindidzaonetsanso chikondi changa pa nyumba ya Israeli, kuti ndingawakhululukire konse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umuche dzina lace Wosacitidwacifundo; pakuti sindidzacitiranso cifundo nyumba ya Israyeli, kuti ndiwakhululukire konse.