Hosea 1:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndidzaonetsa chikondi kwa banja la Yuda, ndipo ndidzaŵapulumutsa ndi mphamvu zanga, Ine Chauta, Mulungu wao. Ndidzaŵapulumutsa osati pochita kumenya nkhondo ndi mauta, malupanga, akavalo ndi anthu okwera pa akavalo ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu ndidzaonetsa chikondi pa nyumba ya Yuda; ndipo ndidzawapulumutsa, osati ndi uta, lupanga kapena nkhondo, kapena akavalo ndi okwerapo ake, koma ine Yehova Mulungu wawo ndidzawapulumutsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndidzacitira cifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.