Hosea 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele ali ngati mpesa wokondwa umene unkabala zipatso zambiri. Chuma chao chikamanka chichuluka, chipembedzo chachikunja chinkakulirakuliranso. Dziko lao likamanka litukuka, iwo ankakometserakometsera mafano ao amene ankaŵapembedza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Israeli anali mpesa wotambalala; anabereka zipatso zambiri. Pamene zipatso zawo zinanka zichuluka, anawonjezera kumanga maguwa ansembe. Pamene dziko lake linkatukuka, anakongoletsa miyala yake yopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Israyeli ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinacurukira zipatso zace, momwemo anacurukitsa maguwa a nsembe ace; monga mwa kukoma kwace kwa dziko lace anapanga zoimiritsa zokoma.