Hosea 10:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kale Efuremu anali ngati ng'ombe yophunzitsidwa imene inkakonda kupuntha tirigu. Tsopano m'khosi lake lokongola ndaikamo goli, kuti agwire ntchito koposa. Ndifuna kuti Yuda azitipula, Yakobe azimwanya mauma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Efuremu ndiye ng'ombe yaikazi yaing'ono, yozereweredwa, yokonda kupuntha tirigu; koma ndapita pa khosi lake lokoma; ndidzamsenzetsa Efuremu goli; Yuda adzalima, Yakobo adzaphwanya chibuluma chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Efereimu ndi mwana wangʼombe wamkazi wophunzitsidwa amene amakonda kupuntha tirigu, choncho Ine ndidzayika goli mʼkhosi lake lokongolalo. Ndidzasenzetsa Efereimu goli, Yuda ayenera kulima, ndipo Yakobo ayenera kutipula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Efraimu ndiye ng'ombe yaikazi yaing'ono, yozereweredwa, yokonda kupuntha tirigu; koma ndapita pa khosi lace lokoma; ndidzamsenzetsa Efraimu goli; Yuda adzalima, Yakobo adzaphwanya cibuluma cace.