Hosea 10:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzifesere m'chilungamo, ndipo mudzakolola madalitso a chikondi changa chosasinthika. Tipulani tsala lanu pakuti nthaŵi yofunafuna Chauta yakwana. Funafunani Chautayo mpaka atabwera kudzakugwetserani mvula ya madalitso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudzibzalire m'chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, navumbitsira inu chilungamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mufese nokha chilungamo ndipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika. Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo; pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova, mpaka Iye atabwera kudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudzibzalire m'cilungamo mukolole monga mwa cifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, nabvumbitsira inu cilungamo.