Hosea 10:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudabzala zolakwa, ndipo mudakolola chilango chake. Mwadya zotsatira zake za mabodza. Chifukwa choti mwadalira magaleta anu, ndi kuchuluka kwa anthu anu a nkhondo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwalima choipa, mwakolola chosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakuti watama njira yako ndi kuchuluka kwa anthu ako amphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma inu munadzala zolakwa, mwakolola zoyipa; mwadya chipatso cha chinyengo. Chifukwa mumadalira mphamvu zanu ndiponso ankhondo anu ochulukawo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwalima coipa, mwakolola cosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakati watama njira yako ndi kucuruka kwa anthu ako amphamvu.