Hosea 10:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adani anu adzakuthirani nkhondo. Malinga anu onse adzaonongedwa monga momwe Salamani adaonongera Betaribele pa tsiku la nkhondo. Adaphwanya azimai pamodzi ndi ana omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribele; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
phokoso lankhondo lidzamveka pakati pa anthu anga kotero kuti malinga anu onse adzawonongeka, monga momwe Salimani anawonongera Beti-Aribeli pa nthawi ya nkhondo; pamene anapha amayi pamodzi ndi ana awo omwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribeli; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ace.