Hosea 10:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Momwemo zidzakuchitikirani inu a ku Betele chifukwa cha uchimo wanu waukulu. Nkhondo ikadzangoyamba m'mamaŵa, nayonso mfumu ya ku Israele idzaphedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo adzakuchitirani Betele, chifukwa cha choipa chanu chachikulu; mbandakucha mfumu ya Israele idzalikhika konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Beteli chifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu. Tsiku limeneli likadzafika, mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo adzakucitirani Betele, cifukwa ca coipa canu cacikuru; mbanda kuca mfumu ya Israyeli idzalikhika konse.