Hosea 10:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtima wao ndi wonyenga. Tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha machimo ao. Chauta adzagumula maguwa ao ansembe, ndipo adzaononga miyala yao yoimiritsa yachipembedzo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtima wawo ndi wonyenga ndipo tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Yehova adzagumula maguwa awo ansembe ndi kuwononga miyala yawo yopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka oparamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.