Hosea 10:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Posachedwa anthuwo adzanena kuti, “Tilibe mfumu tsopano chifukwa sitidamvere Chauta. Komabe mfumuyo ikadatichitira chiyani ife?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo anthuwo adzanena kuti, “Ife tilibe mfumu chifukwa sitinaope Yehova. Koma ngakhale tikanakhala ndi mfumu, kodi mfumuyo ikanatichitira chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti tsopano adzati, Tiribe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzaticitira ciani?