Hosea 10:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Samariya adzachita mantha, fano la mwanawang'ombe la ku Betehaveni likadzaonongedwa. Anthu ake adzalirira. Nawonso ansembe ake aja adzalira maliro a mulungu waoyo, chifukwa ulemerero wake wonse wachokeratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Okhala m'Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni. Anthu ake adzalirira fanolo, chimodzimodzinso ansembe ake adamawo, amene anakondwera ndi kukongola kwake, chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Okhala m'Samariya adzaopera cifanizo ca ana a ng'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ace adzamva naco cisoni, ndi ansembe ace amene anakondwera naco, cifukwa ca ulemerero wace, popeza unacicokera.