Hosea 10:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akachisi opembedzerako milungu yabodza amene Aisraele ankachimwirako, idzaonongedwa. Minga ndi mitungwi zidzamera pa maguwawo. Anthu adzauza mapiri kuti, “Tigwereni!” Adzauza magomo kuti, “Tipsinjeni!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo tchimo la Israele, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa. Ili ndiye tchimo la Israeli. Minga ndi mitungwi zidzamera ndi kuphimba maguwa awo ansembe. Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!” ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo cimo la Israyeli, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni.