Hosea 11:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzaŵabangulira ngati mkango, ndipo anthu anga adzanditsata. Ndidzabanguladi, ndipo adzathamangira kwa Ine ali njenjenje kuchokera kuzambwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kuchokera kumadzulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzatsatira Yehova; Iye adzabangula ngati mkango. Akadzabangula, ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kucokera kumadzulo.