Hosea 11:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Anthu a ku Efuremu andizinga ndi mabodza. Banja limeneli la Israele nlonama kwambiri. Nawonso anthu a ku Yuda akundipandukirabe Ine Mulungu, Woyera ndi wokhulupirika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Efereimu wandizungulira ndi mabodza, nyumba ya Israeli yandizungulira ndi chinyengo. Ndipo Yuda wawukira Mulungu, wawukira ngakhale Woyerayo amene ndi wokhulupirika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Efraimu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israyeli ndi cinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.