Hosea 11:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndikamakangaza kumuitana, iye ndiye kumandithaŵa kunka kutali. Ankaperekabe nsembe kwa Baala ndi kulitenthera lubani fanolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga anawaitana, momwemo anawachokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndimati ndikamapitiriza kuyitana iwo amandithawa kupita kutali. Ankapereka nsembe kwa Abaala ndipo ankafukiza lubani kwa mafano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga anawaitana, momwemo anawacokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema.