Hosea 11:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe ndine amene ndidaphunzitsa Aefuremu kuyenda. Ndidaŵalera, koma sadavomereze kuti amene ndidaŵasamala ndine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Ine ndinaphunzitsa Efuremu kuyenda, ndinawafungata m'manja mwanga; koma sanadziwe kuti ndinawachiritsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi Ine amene ndinaphunzitsa Efereimu kuyenda, ndipo ndinawagwira pa mkono; koma iwo sanazindikire kuti ndine amene ndinawachiritsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Ine ndinaphunzitsa Efraimu kuyenda, ndinawafungata m'manja mwanga; koma sanadziwa kuti ndinawaciritsa.