Hosea 11:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaŵakokera kwa Ine mwachifundo ndi mwachikondi. Ndidaŵanyamula nkuŵatsamiza kutsaya kwanga. Ndidaŵerama, nkuŵadyetsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za chikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira chakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinawatsogolera ndi zingwe zachifundo cha anthu ndi zomangira za chikondi; ndinachotsa goli mʼkhosi mwawo ndipo ndinawerama nʼkuwadyetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za cikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira cakudya.