Hosea 11:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkhondo idzaononga mizinda yao. Adani adzaphwanya zipata za malinga ao ndi kuŵaononga, chifukwa chotsata nzeru zaokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi lupanga lidzagwera midzi yake, lidzatha mipiringidzo yake, ndi kuononga chifukwa cha uphungu wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malupanga adzangʼanima mʼmizinda yawo, ndipo adzawononga mipiringidzo ya zipata zawo nadzathetseratu malingaliro awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi lupanga lidzagwera midzi yace, lidzatha mipiringidzo yace, ndi kuononga cifukwa ca uphungu wao.