Hosea 11:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efuremu? Kodi ndingathe kukutaya bwanji iwe Israele? Kodi ndingathe bwanji kukusandutsa ngati Adima? Kodi ndingathe kukuwononga ngati Zeboimu? Mtima wanga wakana kutero, chifundo changa chikukula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efereimu? Kodi ndingakupereke bwanji iwe Israeli? Kodi ndingakuchitire bwanji zimene ndinachitira Adima? Kodi ndingathe bwanji kukuchitira zimene ndinachitira Zeboimu? Mtima wanga wakana kutero; chifundo changa chonse chikusefukira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakusiya bwanji, Efraimu? ndidzakupereka bwanji, Israyeli? ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zacifundo zanga zilira zonse pamodzi.