Hosea 11:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sindidzalekerera kuti mkwiyo wanga ukulangitse, sindidzamuwononganso Efuremu, pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu. Ine, Woyera uja, ndili nawe, ndipo sindidzabwera kudzakuwononga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sindidzachita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efuremu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sindidzalola kuti ndikulange ndi mkwiyo wanga woopsa, kapena kutembenuka ndi kuwononga Efereimu. Pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu, Woyerayo pakati panu. Sindidzabwera mwaukali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sindidzacita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efraimu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi.