Hosea 12:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Aefuremuwo adaputa mkwiyo wake, nchifukwa chake Chauta adzaŵalanga ndi imfa. Adzaŵalanga chifukwa adamchititsa manyazi kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Efuremu wautsa mkwiyo wowawa, m'mwemo Iye adzamsiyira mwazi wake, ndi Ambuye wake adzambwezera chomtonza chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Efereimu wamukwiyitsa kwambiri. Nʼchifukwa chake Yehova adzawalanga ndi imfa. Adzawalanga chifukwa anamuchititsa manyazi kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Efraimu wautsa mkwiyo wowawa, m'mwemo Iye adzamsiyira mwazi wace, ndi Ambuye wace adzambwezera comtonza cace.