Hosea 12:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani ku Ejipito. Ndidzakukhalitsaninso m'mahema, monga munkachitira masiku amakedzana m'chipululu muja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako chichokere dziko la Ejipito, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a zikondwerero zoikika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa mu Igupto. Ndidzakukhazikaninso mʼmatenti, monga munkachitira masiku aja pa nthawi ya zikondwerero zanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako cicokere dziko la Aigupto, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a masonkhano oikika.