Hosea 13:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kale Aefuremu ankati akalankhula, anthu ankachita mantha chifukwa ankalemekezeka m'dziko la Israele, koma adalakwa popembedza Baala, motero adzafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza m'Israele; koma pamene anapalamula mwa Baala, anafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kale Efereimu ankati akayankhula, anthu ankanjenjemera; anali wolemekezeka mu Israeli. Koma analakwa popembedza Baala, motero anafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Bfraimu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza m'Israyeli; koma pamene anaparamula mwa Baala, anafa.