Hosea 13:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ngati ndidzaŵapulumutsa kwa akufa? Kodi ngati ndidzaŵaombola ku imfa? Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? Anthu ameneŵa sindidzaŵachitiranso chifundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndidzawapulumutsa ku mphamvu ya manda; ndidzawawombola ku imfa. Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? “Sindidzachitanso chifundo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzawaombola ku, mphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako iri kuti? manda, cionongeko cako ciri kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.