Hosea 13:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale kuti Efuremu akondwe ngati bango, mphepo yakuvuma mphepo ya Chauta, idzakuntha kuchokera kuchipululu. Motero kasupe wake adzaphwa, ndipo chitsime chake chidzauma. Adani adzaononga chuma chake chamtengowapatali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ngakhale Efereimu akondwe pakati pa abale ake, mphepo ya kummawa yochokera kwa Yehova idzabwera, ikuwomba kuchokera ku chipululu. Kasupe wake adzaphwa ndipo chitsime chake chidzawuma. Chuma chake chonse chamtengowapatali chidzafunkhidwa ndipo chidzatengedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cinkana abala mwa abale ace, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kucokera kucipululu; ndi gwero lace lidzaphwa, ndi kasupe wace adzauma, adzafunkha cuma ca akatundu onse ofunika.