Hosea 13:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
A ku Samariya adzalangidwa chifukwa choti adapandukira Mulungu wao. Adzaphedwa ndi lupanga, ana ao adzaphedwa moŵakankhanthitsa pansi. Akazi ake apathupi adzang'ambidwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Samariya adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo, chifukwa anawukira Mulungu wawo. Adzaphedwa ndi lupanga; ana awo adzaphedwa mowamenyetsa pansi, akazi awo oyembekezera adzatumbulidwa pa mimba.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wace; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.