Hosea 13:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku ano akuchimwirachimwira. Akudzipangira mafano oumba pogwiritsa ntchito siliva wao. Mafano onsewo ndi ntchito ya anthu aluso. Amati, “Perekani nsembe kwa ameneŵa, pembedzani anaang'ombeŵa poŵampsompsona.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang'ombe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano akunka nachimwirachimwirabe; akudzipangira mafano pogwiritsa ntchito siliva wawo, zifanizo zopangidwa mwaluso, zonsezo zopangidwa ndi amisiri. Amanena za anthu awa kuti, “Amatenga munthu ndi kumupereka nsembe ndipo amapsompsona fano la mwana wangʼombe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano aonjeza kucimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo nchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone ana a ng'ombe.