Hosea 13:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake adzazimirira ngati nkhungu yam'maŵa, kapena mame okamuka msanga. Adzamwazika ngati mungu wouluzika kuchokera pa malo opunthira tirigu, kapena ngati utsi wotuluka pa zenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame asansuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho adzakhala ngati nkhungu yammawa, ngati mame amene amakamuka msanga, ngati mungu wowuluka kuchokera pa malo opunthira tirigu, ngati utsi umene ukutulukira pa zenera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame asansuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi woturuka kukafwambira.