Hosea 13:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti “Ine ndakhala Chauta Mulungu wako kuyambira nthaŵi imene ndidakutulutsa ku Ejipito. Sudziŵa Mulungu wina, koma Ine ndekha, Mpulumutsi wako ndine ndekha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mu Igupto. Simuyenera kudziwa Mulungu wina, koma Ine ndekha, palibe Mpulumutsi wina kupatula Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako cicokere m'dziko la Aigupto, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.