Hosea 13:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵambwandira ngati chimbalangondo cholandidwa ana. Ndidzathyola nthiti zao, ndipo ndidzaŵamwamwata pomwepo ngati mkango, ndidzaŵankhanthula ngati chilombo choopsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung'amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati chimbalangondo cholandidwa ana ake, ndidzawambwandira ndi kuwathyolathyola. Ndidzawapwepweta ngati mkango; chirombo chakuthengo chidzawakhadzula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakomana nao ngati cimbalangondo cocilanda ana ace, ndi kung'amba cokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; cirombo cidzawamwetula.