Hosea 14:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bwererani kwa Chauta, ndipo mumpemphe kuti, “Mutikhululukire machimo athu onse. Mumvere pempho lathu ndipo tidzakuyamikani ndi mau otamanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati ng'ombe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bweretsani zopempha zanu ndipo bwererani kwa Yehova. Munene kwa Iye kuti, “Tikhululukireni machimo athu onse ndi kutilandira mokoma mtima, kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Cotsani mphulupulu zonse, nimulandire cokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati: ng'ombe.