Hosea 14:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzatsitsimutsa Israele ngati mame. Adzachita maluŵa ngati kakombo, adzazika mizu ngati mtengo wa ku Lebanoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzakhala kwa Israele ngati mame; adzachita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yake ngati Lebanoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo. Adzazika mizu yake pansi ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakhala kwa Israyeli ngati mame; adzacita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yace ngati Lebano.