Hosea 14:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene ali wanzeru amvetse zimenezi. Amene ali womvetsa, azisunge. Pakuti njira za Chauta nzolungama, ndipo olungama amayendamo, koma ochimwa amakhumudwamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi. Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi. Njira za Yehova ndi zolungama; anthu olungama amayenda mʼmenemo, koma anthu owukira amapunthwamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? waluntha, kuti adziwe izi? pakuti njira za Yehova ziri zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.